Phokoso pa Kugonana ndi Mlandu Waukulu – A Lawyer Maurice wafotokoza motere
Maurice wapereka chenjezo lamphamvu kwa ma banja omwe amachita phokoso lalikulu akamachita chikondi (kugonana), ponena kuti khalidwe limenelo ndi mlandu ndipo lingawachititse kuti akumane ndi mavuto a malamulo.
Polankhula pa Podcast ya United Showbiz Maurice anafotokoza kuti ngakhale kuli kusonyeza kumva kukoma kapena kukondwa pa nthawi ya kugonana kwachilengedwe, phokoso lopitilira Myezo monga kufuwula mokweza ndi chinthu chokwiitsa anthu ena komanso kusokoneza mtendere wawo.
Iye anatsimikizira kuti ndizololedwa kuti ma banja azisonyeza kumva kukoma kapena kukondwa pomafuula mofatsa pa nthawi ya chikondi, koma adzipewa phokoso lochulukira ndipo azichita izi mwaulemu kwa anzawo apafupi monga oyandikana nawo.
“Simuyenera kufuwula. Kusokoneza mtendere Komanso kumaphatikizapo kupanga phokoso, ndipo aliyense ali ndi ufulu wokhala mwamtendere m’madera awo.”
Lawyer yu anapitiliza kufotokoza kuti kupanga phokoso lalikulu pa kugonana kungaganizidwe ngati kuswa ufulu wa anthu ena amene akumangozimvetsa popanda chilolezo chawo, makamaka m’madera omwe anthu amakhala pafupi kwambiri.
Kuonjezera apo , iye anakumbutsaso makolo ena omwe ali ndi khalidwe losamba limodzi ndi ana achichepere kuti asiye kusamba kapena kuvala m’maso mwa ana awo pakuti ndizolakwika Ndipo ponena za chitsanzo cha milandu ina yomwe inachitikapo ngati yomweyi iye anafotokoza kuti
Mlandu ngati omwewu umu ndim’mene zinakhalira kuti Bambo wina agwidwe ndi kutsekeledwa m’ndende chifukwa chosamba limodzi ndi mwana wake wa Mkazi ndipo mwana wa mkaziyo zinamuopsya zomwe anaonazo mpaka anayamba kuuza anzake kenako nkhani ija inatchuka mpaka ku court Bambo yo ndikutsekeledwa
Izi ndye chaaaaa 😂😂😂😂😂😂
😆😆😆nice song
Aaaaaaa 😅😅
🥱
Eshiiii 😂
Mmmmmm iyiso nde iti sound ija ipeleka chilimbikiso chokwanila kwamamuna
Zuoneka ngat zopanda pake kwa anthu omwe simunakumane nazo mukadzakumana nazo mudzanena😂ndipo or tulo timatheratu ohoo
Ndizoona zimasokoneza ena mukaganizidwe nthawi yomwe akupumulira kuntchito zina
Zokoma
Ok
Awa ndi malamulo aku malawi ubwino wake tonse tikapuma kumwamba basi
Kupanga phokoso kutha kukupangitsa kut ugwidwe ngt ukupanga zimenezo ndi mkazi wamwini
Angogula ma head sets kuti asamave kukuwa.... CHOTI adziwe kukuwa ndi feeling..........chimakhala chimidzi chani enadi anaphudzila koma adakali ndi life yachimidzi 😃😃😃
Km kujoweni kuno nde mungatenge dziko losetu😂🤣
Km ngt Kuli kuphwanya ufulu wa A2 ena ndy lamulo limenero libwere lizagwile ntchito kwambr kuno Ku SA 🤣🤣🤣🤣🤣🤣🤣🤣 Kuli ntchito kuno osat masewera
Aaah nde ikoma bwanj popanda phokoso🤣
🤣🤣🤣makosana ndima lawyer awo tsopano
Anthu a malamulo kuchulusa zochita 😂😂 amzao tisasangalale shuputi